Chuma mzikho zadothi
Chuma mzikho zadothi
John Joseph Matandika
May 31, 2021 · 29 min

Ndi chiyani chimene chimapangitsa mpingo kukhala opambana?

MP3

Lero tikufuna tione chimene chimapangitsa mpingo kukhala opambana. Ndiye poyamba tiyeni tione kuti kodi ndi chiyani chimene chimapanga mpingo kukhala osiyana ndi mabungwe ena achikhristu?

Poyankha funso limeneli ndiwelenge mutu 29 wa Chivomelezo cha ku Belgium chimene chidalembedwa m’chaka cha 1567 ndi Guido de Bres amene adali m’laliki m’mipingo ya chikonzedwe ku Netherlands ndipo adaphedwa chifukwa cha chikhulupiliro chake m’chaka chomwecho.

Chimene chidachitika ndi chakuti, nthawi imeneyi mipingo yak u Netherland inali pa chizuzo choopsya ndi utsogoleri wa boma wa chiroma. Ndiye ngati gawo limodzi lolimbana ndi kuzuzidwa kwawoko, komanso kuonetsela kwa owazuzawo kuti mipingo ya chikozedwe si anthu ogalukila, monga m’mene amawayimbila mlandu, koma kuti iwo anali nzika zotsatila malamulo a dziko amene amatsatila chiphuzitso cha chikhristu choona monga mwa Mawu a Mulungu, nkulu ameneyu de Bres adakoza chivomelezo chimenechi m’chaka cha 1561.

Mawu ochokera ku chivomelezo cha ku Belgium, mutu 29:

“Mpingo woona utha kudziwika ngati uli ndi zizindikilo izi: mpingowo umakangalira nkulalikila kwa mawu kwenikweni; umagwilitsa ntchito masakaramenti moyenelera monga m’mene Khristu adawakhazikitsila; komanso umachita chidzudzulo cha pa mpingo kukoza zolakwika.”

Ndiye monga chivomelezo chakale cha chikozedwe chimenechi, pali zinthu zitatu zimene zimaonetsela mpingo woona. Zizindikilo zimenezi sikuti zimationetsela zinthu zonse zimene mpingo umasowekela kuti ukhale ndi umoyo wabwino, koma zimationetsela kuti kodi gulu limene likudziwika ndi dzina limeneli nkowayeneladi kugwilitsa ntchito dzinali. Ndiye tiyeni tione chizindikilo chilichonse pachokhapachokha.

This podcast uses Anchor (from Spotify) for stats, tracking, and dynamic audio. What this means Episodes play from the podcast's own servers, unmodified. Not affiliated with Podbay.