
Ndi chifukwa chiyani tili ndi ma translation ambiri?
Ndiye ndi chifukwa chiyani tili ndi ma translation ambiri?
Monga ndinanena kale, Monga ndinanena kale, anthu ena amaganiza kunena kuti kupezeka kwa ma translation ambiri kumatsimikizila kuti Baibulo lili ndi zolakwika zambiri, koma tiyeni tione nkhani imeneyi mozama. Ndiyambe ndi kufusa funso ili, kodi Mose amawerenga translation yanji ya Baibulo? Yankho ake ndi lakuti, padalibe Baibulo la Mose. Timadziwa kuti Mose adalemba mabuku asanu oyambilira a Baibulo amene amatchedwanso Pentatuku, adalemba atatuluka ku Egypt ndipo pa gawo lalikulu la moyo wake adalibe mabuku asanu amenewa. Adali ndi timagawo, koma osati monga tili nalo lero lino. Imfa yake ikulembedwa pa Deuteronomy 34, zimene zikuonetsa kuti sakadalemba chapter chomaliza cha Pentatuku. Ambiri amakhulupilira kuti Yoswa ndiye adalemba chapter chomalizachi.
➢ Tidaonapo za kagawidwe kena ka Baibulo mu phuzilo lathu la m’mbuyo koma mabuku 66 amene ali mu Baibulo kudalibe nthawi ya Mose ngakhale Yesu. Kuchokela nthawi imene Genesis adalembedwa kudzafika nthawi imene Chivumbulutso amalembedwa padadutsa zaka pafupifupi 1,500.
➢ Tikumbukile Baibulo lidalembedwa ndi Mulungu, ndipo Mulunguyo adagwilitsa ntchito anthu pafupifupi 40 kulemba Baibulo.
➢ Chipangano chakale chidalembedwa m’chiheberi komanso Aramaic pang’ono mu buku la Daniel komanso Ezara. Chipangano chatsopano chidalembedwa mu chi Greek.
➢ Kuonjezela pamenepo, Baibulo m’mene limalembedwa lidalibe ma chapter, ma vesi, mau otsogolera ndi ena oonjezeledwa ndi anthu litalembedwa kale.
➢ Ndiye tiyeni tibwelere ku funso lathu loyamba, potengela zinthu zimene ndafotokozazi, kodi mukuganiza kuti tingaliyankhe motani – ndi chifukwa chiyani tili ndi ma translation ambiri?
➢ Poyamba titha kunena kuti, popeza anthu ambiri lero lino salankhula chiheberi, Aramaic kapena Greek, amene amadziwa zilankhulo zimenezi adatanthauzila.
➢ Chimene mukuyenela kudziwa ndi chakuti Baibulo tili nalo lero lino lidatanthauzilidwa bwino komanso modalilika zimene zidasungidwa bwino mu nkhani ndi m’zolemba zosiyanasiyana.
➢ Koma, zilipo nthawi zimene tikalingalira m’mene Baibulo lidalembedwela zimene zitha kutipangitsa kulikayikila. Poyamba, mukuyenela kutsimikizika kuti Baibulo Mawu enieni a Mulungu, ndipo kuti Mulungu adzasamalira Mawu ake. Kupezeka kwa ma Baibulo lero lino ndi umboni wa chisamaliro cha Mulungu mwa chisomo.
➢ Kachiwiri, pali umboni waukulu mu mbiri yotsimikizila za kulunjika komanso kudalilika kwa Baibulo. Si buku limene tingalikayikile. Pali ma umboni akuluakulu mu mbiri komanso ngakhale archaeology zimene zitipangitse kuchita nalo chidwi Baibulo.
This podcast uses Anchor (from Spotify) for stats, tracking, and dynamic audio. What this means Episodes play from the podcast's own servers, unmodified. Not affiliated with Podbay.
