
Kodi Baibulo timawerenga motani?
Ndiye tiyeni tifike pa funso lakuti: kodi Baibulo timawerenga motani? Litha kuoneka ngati funso lodabwitsa kwambiri popeza ambiri mwina timadziwa kuwerenga Baibulo. Koma chimene tikufuna tione ndi chakuti, Baibulo ndi losiyana ndi mabuku ena onse amene adalembedwa, ndi chifukwa chake akhristu akuyenela kufikila kuwerenga Malemba Opatulika mosiyanitsa ndi mabuku ena.Chinthu choyamba chimene tikufuna tichione ndi chakuti, tikuyenela tiwerenge Baibulo mwauzimu.Ahebri Ø Ndiye chinthu chimodzi chimene tikuphuzila pa ndime imeneyi ndi chakuti Mawu a Mulungu ndi amoyo. Mawu amaonetseladi kuti ndi amoyo ndipo ali ndi kuthekela kuweruza mtima wanu komanso kukubweletsani poyera.Ø Kachiwiri, popeza kuti buku ndi la moyo ndipo timakhulupilira moona mtima kuti umu ndi m’mene Mulungu amalankhulira nafe, tikuyenela kulifikila mwa ulemu onse.Ø Pali njira zambiri zimene tingathe kufikila mwaulemu, koma njira yoyambilira ndi kufikilako mwakupemphela.Ø Kumbukilani zinthu zitatu zimene tidaona zokhudzana ndi Malemba Opatulika pa phuzilo lachiwiri lija: kuti Baibulo lidauzilidwa, lilibe cholakwa ndipo lilibe chophonyetsa china chilichonse. Komanso tidaona kuno ndi lopanda malire.Ø Tiyeni tiwerenge Yesaya Ø “…mawu a Mulungu wathu adzayima kwamuyaya.”
This podcast uses Anchor (from Spotify) for stats, tracking, and dynamic audio. What this means Timestamps may be slightly off because ads are inserted dynamically. Episodes play from the podcast's own servers, unmodified. Not affiliated with Podbay.
